BULLETS YAPEZEKA NDI MILANDU ITATU
Bungwe la Football Association of Malawi lapeza milandu itatu kuti timu ya FCB Nyasa Big Bullets iyankhepo pa zomwe zinachitika pa masewero awo ndi Mzuzu City Hammers.
Mlandu woyamba ndi woti Bullets inakanika kuletsa ochemerera awo kuchitira chipongwe, kumenya ndi kufika malo oletsedwa komanso kuletsa achitetezo kugwira munthu yemwe analowa mu bwalo la zamasewero.
Wachiwiri ndi kulimbana komanso kugwiragwira oyendetsa mpira ndipo wina ndi wobweretsa masewero a mpira ku zipolowe.
FAM yapezanso masapota asanu, Chingeni Gumbala Kadam’manja, Shaibu Woyera, Trouble Ndikida Kapito, Alick Tsegula, Ganizani Baba ndi Dyton Bello omwe ankalimbana ndi Hammers polowa ndi nthawi yopumira powaopseza.
Timuyi yapatsidwa maola 48 kuti iyankhepo pa milanduyi. Bullets inapambana masewero 2-0 kuti ifike mu ndime yotsiriza.
Photo - MH Photography
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores