Katswiri wa Mighty Wanderers, Stanley Sanudi, atha kupita kunja kwa dziko lino koyamba pomwe akufunidwa ndi timu ya Caps United yaku Zimbabwe.
Sanudi sanatumikirepo timu ya kunja kwa dziko angakhale kuti ndi osewera wapamwamba mu zaka zonse zomwe wakhala akusewera ndipo wasewerera timu ya dziko lino masewero odutsa 80.
Timu ya Caps ili ndi anyamata awiri a mdziko muno, Chawanangwa Kaonga ndi Lloyd Njaliwa komanso wachiwiri kwa mphunzitsi wawo ndi Joseph Kamwendo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores