FPA yayika malire ochotsera osewera
Bungwe loyang'anira osewera la Football Players Association layika tsiku la 28 February 2026 kukhala lomaliza loti matimu achotsere osewera omwe sakuwafuna pofuna kuti akwanitse kupezanso matimu atsopano.
Mlembi wa bungweli Ernest Mangani wati matimu ambiri amachotsa osewera nthawi yoti msika watsekedwa zomwe zimawachititsa kusowa kosewerera komanso matimu abwino.
"Ndi chifukwa chake tikupempha matimu komanso kukakamiza kuti osewera akwanitse kupezanso matimu abwino chifukwa kuwachedwetsa ndi kuwaphera ufulu," Iye anatero.
Iye wamema osewera kuti alowe bungwe lawoli kuti mawu awo azimveka ndipo wati akambirana ndi Football Association of Malawi kuti osewera onse amu Supa ligi alowe bungwe lawo.
Bungweli limaunikira za ufulu ndi umoyo wa osewera ndipo osewera yemwe ali ndi mgwirizano ndi timu atha kukhala membala wawo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores