''NDI ZOVUTA KUGWIRA OSEWERA PA 24 DECEMBER NDI KHRISIMASI'' - MSUKWA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Mapopa Msukwa, wati ali ndi nkhawa kuti masewero awo apa tsiku lomaliza sadzayenda monga momwe akufunira kamba koti osewera samagwirika mu nyengo ya zisangalalo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Mzuzu City Hammers 3-0 kuti afanane mapointsi ndi FCB Nyasa Big Bullets ndipo wati akufunitsitsa atathera pa nambala yachiwiri koma masewerowa adza mu nyengo ya chisangalalo.
''Tikuyang'ana kuti tidzachite bwino pa masewerowa komabe akubwera mu nthawi ya Khristimasi ndipo lero ndi pa 24 [December] zomwe zimakhala zovuta kumugwira osewera nde zidzaoneka,'' anatero Msukwa.
Silver ili pa nambala yachitatu mu ligi ndi mapointsi okwana 63 pa masewero 29 omwe yasewera ndipo yapambana ka 18, kufanana mphamvu kasanu ndi kanayi ndi kugonja kawiri kokha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores