FAM YALAMULA BULLETS KULIPIRA K5 MILLION
Bungwe la Football Association of Malawi lalamula timu ya FCB Nyasa Big Bullets kulipira ndalama zokwana K5 million kamba ka zachisokonezo zomwe anachita pa masewero omwe anagonja 1-0 ndi Mighty Wanderers pa 2 November 2025.
Bungweli lachita izi litayipeza timuyi yolakwa pa milandu yomwe anayipeza nayo ndipo timuyi inavomera. Zilango zili motere:
•Bullets ilipire K1 million kamba koti ochemerera awo anagenda wachiwiri kwa othandizira oyimbira pa mphindi 50 ndipo masewero anayima kwa mphindi zitatu.
•Bullets ilipire K2 million poti mmodzi mwa opereka chitetezo watimuyi, a Thomson Chauluka anapita pagolo la Wanderers kukathira zinthu za madzi pa mphindi 96 za masewerowa.
•Bullets ilipire K2 million kamba kolowetsa zipolowe ku mpira posaletsa ochemerera awo kugenda komanso wachitetezo wawo kulowa mu bwalo.
Ndipo a Chauluka apatsidwa chilango chosaonekanso ku masewero kwa miyezi 12 kamba komenya Dalitso Khungwa pa masewerowa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores