CHIMBAMBA WAYAMBA ZOKONZEKERA KU BULLETS
Wachiwiri kwa mphunzitsi kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Gilbert Chirwa wati goloboyi watimuyi, Richard Chimbamba wayamba kuchita zokonzekera patsogolo pamasewero a timuyi ndi Kamuzu Barracks Lachinayi likudzali pabwalo la Civo.
Chimbamba wakhala asakupezeka kutimuyi pa zifukwa zokhudzana ndi kusowa mwambo pomwe zinamveka kuti anakana kupepesa atachedwa kuzokonzekera za timuyi.
Koma polankhula pamsonkhano wa olemba nkhani patsogolo pamasewero awo ndi KB, Chirwa anatsimikiza kuti tsopano Chimbamba wabwelera pabwalo la zamasewero, komabe Innocent Nyasulu ndi goloboyi woyamba kutimuyi kapena kuti 'first choice goalkeeper' pachingelezi.
"Chiganizo cha yemwe ayambe chili m'manja mwa aphunzitsi." Iye anaonjezera.
Mwazina, Chirwa anati Aaron Chilipa sapezeka pamasewerowa kaamba koti akadali ovulala ndipo Chikumbutso Salima, yemwe zimakaikitsa ngati apezeke pamasewerowa, tsopano alibwino ndipo apezeka nawo.
Pakadali pano, timu ya FCB Nyasa B
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores