"Masewero akungolowanalowana kanthawi kochepa" - Mpinganjira
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers, Bob Mpinganjira, wati timu yake yakonzekera bwino masewero awo ndi timu ya Ekhaya komabe akusewera masewero ochuluka kwambiri mu kanthawi kochepa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko lachitatu pa bwalo la Kamuzu ndipo wati akudziwa kufunikira kwa masewerowa kuti apeze chipambano.
"Ekhaya ikuchokera kolepherana ndi Dedza Dynamos kusonyeza kuti chipambano akuchifuna kwambiri koma takonzekera bwino ngakhale kuti nthawi yokonzekera ndi yochepa poti masewero akungolowanalowana," iye anafotokoza.
Iye watinso Emmanuel Nyirenda komanso Rajab Nyirenda apezeka pa masewerowa pomwe Wisdom Mpinganjira ndi Gaddie Chirwa sapezeka kamba kovulala.
Wanderers ili pamwamba pa ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 51 pa masewero 21 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores