"Chigawo choyamba anatichinya apa tsopano tiwachinye" - Chirwa
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Gilbert Chirwa, wati wauza osewera ake kuti adzaike mtima pomwe akudzakumana ndi timu ya Mighty Wanderers ndi cholinga choti adzapambane pa masewerowa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa MAFCO 3-0 lachiwiri pa bwalo la Kamuzu ndipo amaunikirapo momwe akuwaonera masewerowa omwe aliko lamulungu pa bwalo lomweli.
Iye wati timu yake inamva kupweteka kwambiri itagonja mu Chigawo choyamba ndi Manoma koma apa tsopano ayesetsa kuti adzapeze chipambano.
"Tawauza anyamata kuti adzalimbikire ndi kuyikirapo mtima kuti masewero awawa tsopano tidzawachinye nde tikonzekera bwino ndithu kuti zidzatiyendere," anatero Chirwa.
Iye anayamikira osewera ake kamba kosewera mwapamwamba ndi MAFCO kuthandiza kuti atsegule mpaka wa mapointsi asanu ndi awiri pa mtunda pa ligi.
Bullets ili ndi mapointsi okwana 49 itapambana ka 16, kufananitsa mphamvu kamodzi ndi kugonja katatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores