BULLETS ILIBE YANKHO NDI MAFCO
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yatsimikiza kuti wosewera pakati, Yankho Singo sapezeka pamasewero omwe timuyi isewere ndi MAFCO FC Lachiwiri muligi ya TNM.
Polankhula pa msonkhano wa olemba nkhani Lolemba, wachiwiri kwa mphunzitsi kutimuyi, Gilbert Chirwa anati Singo anavulala minyewa pamasewero omwe timuyi inagonjetsa Kamuzu Barracks 2-1 muchikho cha FDH Bank Loweruka.
Mwazina, Chirwa anati Babatunde Adepoju, Chikumbutso Salima komanso Innocent Nyasulu omwe anawapumitsa pamasewero awo ndi KB, apezeka pamasewerowa.
Timu ya Bullets ikupita m'masewerowa ikutsogolera mndandanda wa momwe matimu akuchitira muligi ya TNM ndimapointi 46 pamasewero 19 pamene MAFCO FC ili panambala 11 ndimapointi 23 pamasewero 20.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores