"AMWENE NDI PENDAPENDA PENDAPENDA BASI" - ABAMBO
Mkulu woyang'anira aphunzitsi kutimu ya Mighty Tigers, Robin Abambo Alufandika, wavomereza kuti timu yake ikuyenda mwa pendapenda mu ligi ya chaka cha 2025.
Iye amayankhula izi kutsatira kuvutika kwa timuyi pomwe yagula malo mu matimu otuluka mu ligi chifukwa ili pa nambala 14.
Pa masewero 19, timuyi yapambana kanayi kokha, kufanana mphamvu kasanu ndi kugonja ka khumi kuti akhale ndi mapointsi 17 ndipo akuperewera mapointsi atatu kuti atulukemo mu chigwa cha imfachi.
Abambo ati zinthu zikuvutadi koma ayesetsa kuti pa masewero khumi ndi amodzi omwe atsala nawo mu ligiyi achiteko bwino ndithu.
"Amwene ndi pendapenda pendapenda basi. Momwe ndanenera kuti pendapenda Koma amati pendapenda si kugwa Koma kuchalira ulendo nde tiona kuti ulendowu tiuyenda motani," anatero Abambo.
Tigers ndi imodzi mwa timu yomwe yakhalitsa mu ligiyi ndipo imaposa matimu ochuluka kwambiri poti inatengako supa ligi mu chaka cha 1989.
Wolemba : Hastings Wadza
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores