"SAMA WATSALIRA PANG'ONO BOLA NYONDO" - MPINGANJIRA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers, Bob Mpinganjira, wati anyamata atatu omwe anali ovulala, Sama Thierry Tanjong, Clement Nyondo ndi Richard Chipuwa abwerera kutimuyi ndipo ngati angachite bwino atha kusewera nawo ndi timu ya Dedza Dynamos.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa lamulungu mu boma la Dedza lamulungu ndipo wati ngakhale zili chomwechi, Sama Thierry Tanjong watsalirabe pang'ono kuti achilitsitse.
"Osewera monga Gad Chirwa, Mphatso Kamanga komanso Chimwemwe Nkhoma akadali ovulala Koma Sama, Chipuwa ndi Nyondo alibwino komabe ali mmanja mwa madotolo kuti ngati akhale bwino tiwaona mmasewerowa," anatero Mpinganjira.
Patsogolo pa masewerowa, Iye wati timuyi yakonzekera bwino pa masewerowa kuti akwanitse kutenga mapointsi atatu omwe awathandize kupita patali mu ligi.
Manoma ali ndi mapointsi okwana 39 pa masewero 17 omwe asewera mu ligi ndipo ali pa nambala yachiwiri kuchepekedwa ndi mapointsi anayi ndi Bullets.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores