Babatunde watengedwa ku Flames
Katswiri womwetsa zigoli kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Babatunde Adepoju, wayitanidwa kutimu ya dziko ndi Kalisto Pasuwa patsogolo pa masewero opitira ku World Cup omwe aliko mwezi uno.
Bungwe la Football Association of Malawi ndi lomwe latsimikiza za nkhaniyi pomwe Iye anasiyidwa pa ndandanda oyamba omwe Pasuwa anatulutsa.
Babatunde akalowa mmalo mwa Gabadinho Mhango yemwe sapezeka pa masewero oyamba a Sao Tome and Principe kamba kokhala ndi ma kadi achikasu koma adzapezeka pa masewero achiwiri ndi Equatorial Guinea.
Aka akakhala koyamba kuti osewerayu ayitanidwe kutimuyi kutsatira kupatsidwa mapepala okhalira mzika ya dziko lino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores