Chitipa ipereke K6 million ku SULOM
Komiti yokhazikitsa bata ku bungwe la Super League of Malawi lapereka chilango kutimu ya Chitipa United kuti ipereke ndalama zokwana K6 million Kamba ka milandu yomwe anapalamula pomwe ankakumana ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets.
Timuyi yapezeka yolakwa pa mlandu obweretsa chisokonezo ku masewero a mpira pomwe ochemelera awo anaonedwa akuponya miyala pa bus ya Bullets komanso kuti Mphunzitsi wawo anachita zosokoneza.
Ndipo Kondwa Ikwanga wauzidwa kusapezeka pa bwalo kwa masewero atatu kamba ka mchitidwe wake pa masewerowa.
Mmasewerowa, timuyi sinakhutire ndi kayimbilidwe ka oyimbira pa masewerowa pomwe anagonja 2-0.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores