Wanderers inyamuka lero
Timu ya Mighty Wanderers ikunyamuka m'dziko muno lero kupita ku Francistown m'dziko la Botswana lero pomwe akuyembekezeka kukumana ndi timu ya Jwaneng Galaxy mu masewero achibwerenza amu chikho cha CAF Confederations Cup.
Timuyi ikuyembekezeka kugwiritsa ntchito ndege yawoyawo yomwe ithandizire kuti osewera a timuyi asakhale otopa patsogolo pa masewerowa.
Anthu okwana 52 omwe ndi osewera, aphunzitsi ndi akulu-akulu atimuyi akhale nawo pa ulendowu umene akunyamuka nthawi ya 10:30hrds kummawaku.
Osewera ena monga Sama Thierry Tanjong, Mphatso Kamanga komanso Richard Chipuwa omwe akhala ali ovulala akuyembekezeka kukhala nawo pa ulendowu pomwe amachita zokonzekera ndi timuyi.
Manoma anapambana 1-0 mu masewero awo oyamba ndi chigoli cha Felix Zulu pa mphindi 80.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores