Nyambose wakondwa ndi kaseweredwe ka Songwe
Mphunzitsi watimu ya Songwe Border United, Christopher Nyambose, wati ndi wokondwa ndi momwe timu yake yasewerera ndi Kamuzu Barracks ndipo wati wayamba kulimba mtima kuti chomwe akufuna kupanga chayamba kutheka.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 pa bwalo la Champions ndipo wati timu yake inataya mipata yochuluka kuphatikiza penate imene anaphonya komabe ndi momwe yasewerera ikulimbitsa mtima kuti chomwe akufuna chitheka.
"Anali masewero abwino omwe tinayesetsa kutchinga bwino kuti KB isagoletse ndipo tinapeza mipata tambiri kuphatikizapo penate yomwe tinaphonya ndipo mchigawo chachiwiri tinakanika kutchinga nde anzathu anachinya komabe ndiyamikire anyamata anali bwino." Iye anatero.
Nyambose wati maso ake wayika kuti asatuluke mu ligi ndipo ayesetsa kuti apeze mapointsi omwe atha kuwasunga mu ligiyi ndipo maso ayika pa masewero awo ndi FCB Nyasa Big Bullets.
Iwo ali ndi mapointsi awiri atalepherana kawiri ndi kugonja ka 1
Wojambula : Civil Service United media
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores