"Sitimayenera kutaya ma pointsi lero" - Kananji
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Eliya Kananji, wati timu yake imayenera kupambana mu masewero awo ndi timu ya Civil Service United Koma kuti ataya mipata yochuluka yomwe anakwanitsa kupeza.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 0-0 pa bwalo la Aubrey Dimba ku Mchinji ndipo wati mwayi anali nawo oti akanatha kumaliza masewerowo Koma anaphonya kwambiri.
"Mu Chigawo choyamba tinapeza mipata yochuluka kwambiri yomwe tikanatha kuwamaliza masewero Koma tinaphonya, mchigawo chachiwirinso tinapeza ingapo kenako kumapeto tinatayilira moti tikanatha kuchinyitsa." Anatero Kananji.
Iye wati waona mavuto omwe timuyi yakumana nawo mmasewerowa komanso zabwino zomwe anachita mmasewerowa azipitiliza pa masewero awo ndi Mighty Wanderers omwe aliko lachitatu sabata ya mawa.
Creck Sporting Club ili pa nambala 10 mu ligi pomwe ili ndi ma points 19 pa masewero 16 pomwe yapambana kasanu, kulepherana kanayi ndi kugonja kasanu ndi kawiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores