Timu ya Mighty Wanderers Reserve yamaliza pa nambala yachiwiri mu ligi yaku Chigawo cha kummwera ya Thumbs Up kutsatira kupambana 2-0 ndi timu ya Immigration lachinayi ku bwalo la Mpira.
Timuyi inagonjetsa zigoli zawo kudzera mwa Chastrey Kandiado komanso Bobson Jr kuti apeze chipambanochi ndi kusuntha pa ndandanda wa matimu mu ligiyi.
Timuyi tsopano ili ndi mapointsi 32 pa masewero 15 omwe yasewera kutengera kuti yapambana kasanu ndi kanayi, kufanana mphamvu kasanu komanso kugonja kamodzi.
Iwo akuchepekedwa ndi point imodzi kuti ayipeze Ekhaya Reserve yomwe ili pamtunda komanso yatsala ndi masewero amodzi pomwe matimu ngati FCB Nyasa Big Bullets Reserve sangayipeze Wanderers angakhale kuti nawo atsala ndi masewero amodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores