NKHANI
Sipikala wa nyumba ya malamulo, Catherine Gotani Hara, anayitana timu ya Mzuzu City Hammers kumadyerero kunyumba kwake poyithokoza mmene yachitira mu chaka cha 2024.
A Gotani anayitana timuyi lachisanu ku nyumbayi mu mzinda wa Mzuzu kutsatira kumaliza mu nambala yachinayi mu ligi komanso kufika mu ndime yotsiriza ya chikho cha Castel Challenge Cup chomwe anagonja 1-0 ndi Mighty Mukuru Wanderers mu ndime yotsiriza.
Mlembi wamkulu watimuyi, Benjamin Thole, wathokoza a Gotani kamba ka mwambowu ndipo wati izi zimalimbikitsa osewera kuti adzachitenso bwino mu chaka cha mawa.
Timuyi inasankhidwanso kukhala timu yomwe yachita bwino kwambiri pamatimu onse akumpoto pa mphoto za Mpoto awards mu mwezi wa December womwewu.
Source: Avant Publications
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores