"TISAYEMBEKEZERE ZAMBIRI KWA SILVER NDI WANDERERS" - MITAMBO
Mmodzi mwa anthu oyankhulapo pa nkhani za masewero mdziko muno, Justin Mitambo, wati ngati dziko tisayembekezere zambiri pa Silver Strikers ndi Mighty Mukuru Wanderers ngati angalowe mu mipikisano ya CAF.
Iye amayankhula pomwe matimu onsewa awonetsa chidwi chofuna kusewera mu mipikisanoyi pomwe ali ovomerezeka kusewera mmalingana ndi momwe achitira chaka chino.
Silver Strikers ikhonza kutenga mbali mu CAF Champions League kamba koti inatenga ligi pomwe Wanderers itha kusewera mu CAF Confederations Cup potenga chikho cha Castel Challenge Cup ndipo matimu onse awonetsa chidwi chofuna kutenga mbali.
Koma Mitambo wati tisayembekezere zambiri poti mdziko muno matimu amakanika kupita patali poti osewera ambiri samasewerasewera mu mipikisanoyi.
"Kwa zaka zingapo zapitazi takhala tikuvutika kuti tifike mu magulu kamba koti osewera omwe tili nawo samasewerasewera mpikisanowu bola titapeza ena akunja ndekuti zidzatithandiza." Anat
Iye watinso izi zipindulira osewera a mmatimuwa kuti akaonedwenso kunjako ngati momwe zidachitira Lanjesi Nkhoma ndi Patrick Mwaungulu ndipo zoterezi zimathandizira kwambiri timu ya dziko lino.
Matimu a FCB Nyasa Big Bullets, Wanderers, Silver Strikers ndi Masters Security ndi omwe akhala akutenga nawo mbali mu mipikisanoyi chichokereni chaka cha 2016.
Admin mwayamba chinyengo, shadrek game ya pa 18/12/2024 yomwe ndi ya arsenal vs crystal palace inathela 3-2 koma amene analosela molondola ndi gito bento yekha basi osati shadrek kapena aida. ndipo shadrek analosela 2-1, aida analoselaso 2-1, dami analosela 3-1. Zomwe zikutanthauza kuti aida ndi shadrek mwangowakokela popanda game. Koma zenizeni ndiizi top 3 magame aloseledwa motele kuyambi pa 16/12/2024 mpaka pa 22/12/2024 1-dami.maliyo 11 games 2-aida.ernesto 10 games ndipo 3-shadrek 9 games. TOP 2 dami.maliyo ndi aida.ernesto awa ndamene agawane k30000. dami.maliyo k20000. aida.ernesto k10000. SITIKUFUNA ZACHINYENGO IFE PANO.
ZOONA PAYAMBA KUENDA CHINYENGO
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores