"TISAYEMBEKEZERE ZAMBIRI KWA SILVER NDI WANDERERS" - MITAMBO
Mmodzi mwa anthu oyankhulapo pa nkhani za masewero mdziko muno, Justin Mitambo, wati ngati dziko tisayembekezere zambiri pa Silver Strikers ndi Mighty Mukuru Wanderers ngati angalowe mu mipikisano ya CAF.
Iye amayankhula pomwe matimu onsewa awonetsa chidwi chofuna kusewera mu mipikisanoyi pomwe ali ovomerezeka kusewera mmalingana ndi momwe achitira chaka chino.
Silver Strikers ikhonza kutenga mbali mu CAF Champions League kamba koti inatenga ligi pomwe Wanderers itha kusewera mu CAF Confederations Cup potenga chikho cha Castel Challenge Cup ndipo matimu onse awonetsa chidwi chofuna kutenga mbali.
Koma Mitambo wati tisayembekezere zambiri poti mdziko muno matimu amakanika kupita patali poti osewera ambiri samasewerasewera mu mipikisanoyi.
"Kwa zaka zingapo zapitazi takhala tikuvutika kuti tifike mu magulu kamba koti osewera omwe tili nawo samasewerasewera mpikisanowu bola titapeza ena akunja ndekuti zidzatithandiza." Anat
ZOONA PAYAMBA KUENDA CHINYENGO
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores