"YAKWANA NTHAWI YOKABWENZERA 8-0 IJA" - THOLE
Mlembi wamkulu wa timu ya Mzuzu City Hammers, Benjamin Thole, wati nthawi yakwana kuti timu yake ikabwenzere zowawa zomwe anamva mu chigawo chachiwiri cha ligi pomwe anagonja 8-0 ndi Mighty Mukuru Wanderers ndipo sakafikitsanso ku mapenate.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Manoma mu ndime yotsiriza ya chikho cha Castel Challenge loweruka masana pa bwalo la Bingu ku Lilongwe.
Iye wati aphunzitsi anaona zofooka zonse za timuyi ndipo nthawi yakwana kuti Manoma amve zowawa mu chakachi pomwe awabwenzere chipongwe chapa bwalo la Kamuzu.
"Tiwameme anthu abwere adzaone tikutenga chikho pa Bingu. Nthawi yakwana yokha kuti tibwenze 8-0 uja ndipo awa tikamaliziratu mu mphindi 90." Anatero Thole.
Timuyi inatulutsa timu ya Karonga United mu ndime ya matimu asanu ndi atatu ndipo inagwetsanso FCB Nyasa Big Bullets mu ndime ya matimu anayi mmasewero onsewa ku mapenate kuti afike ndime yotsiriza.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores