"TIKUYENERA KUCHOTSA ZINTHU ZINA POTI TIKUMAONEKA PA FIFA" - ZAKAZAKA
Mkulu woona za mipikisano ku bungwe la Football Association of Malawi, Gomegzani Zakazaka, wati pakuyenera kuchotsa zinthu zina mu mpira wathu ngati za zikhulupiliro komanso chipolowe poti dziko lonse lapansi likumaonera masewero a mdziko muno.
Iye amayankhula patsogolo pa ndime yotsiriza ya chikho cha Castel Challenge masana a loweruka pomwe wati akuyembekezera kukamaliza bwino mu chaka cha 2024.
"Tikufuna tikamalize mwapamwamba mu ligi ya chaka chino kuti tinali ndi chaka chopanda za chiwawa ngakhale pena ndi pena sizimalephera koma kwakukulu tingochotsa zinazo chifukwa mpira wathu ukumaoneka pa FIFA." Iye anatero.
Iye anati ngati khalidwe likhale lopambana ndekuti anthu azisilira mpira wathu kupangitsanso kuti osewera athu akhale ndi mwayi kunja kwa dziko lino.
Ndime yotsiriza ya chikho cha Castel iseweredwe pakati pa matimu a Mighty Mukuru Wanderers komanso Mzuzu City Hammers pa bwalo la Bingu mu mzinda wa L
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores