"BWERANI MUDZAONE TIKUSINJA BULLETS PAKWAWO" - THOLE
Mlembi wamkulu watimu ya Mzuzu City Hammers, Benjamin Thole, wati timu yake ipange kanthu kena kozwizwitsa pomwe agonjetse timu ya FCB Nyasa Big Bullets pakwawo kuti afike mu ndime yotsiriza ya chikho cha Castel Challenge.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo omwe ali pa bwalo la Kamuzu lachiwiri mu ndime ya matimu anayi ndipo wati timu yake yakonzeka kwambiri kuti agwetse Bullets.
Iye wati alibe mantha oti Bullets ili pa kwawo poti mpira umenewu unatha kalekale ndipo Iwo apita kukangogwira ntchito nkumabwera.
"Tiwameme anthu kuti abwere, chabwino masewero ayikidwa tsiku loyipa komabe abwere adzangoona mmene titawatulutsire a Bullets mu Castel." Anatero Thole.
Timuyi inagonjetsa Karonga United 3-2 pa mapenate ikuti ifike mu ndime yamatimu anayi a mpikisanowu ndipo opambana pa masewero awowa akakumana ndi Mighty Mukuru Wanderers mu ndime yotsiriza.
Akunama amenewa bullets pipe moto moto anabachepa
Kkkkkkkk bullets ikuwina timwa wa mkaka moto kt 🔥🔥🔥🔥🔥
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores