"ANKHALAKALE SAKUTITHANDIZA KOMA MUMALOZA MPHUNZITSI" - MPULULA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Tigers, Leo Mpulula, wati ndi zomvetsa Chisoni kuti anthu amaloza chilichonse mphunzitsi wamkulu koma osewera omwe analiko kale kutimuyi palibe chimene akuchita ndipo akudalira akutimu yawo yachisodzera.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 5-0 ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Kamuzu ndipo wati agonja osati kuti Wanderers ilibwino koma kuti iwowo salibwino.
Iye wadandaula kuti pofikira panopa, osewera akuluakulu kutimuyi akukanika kuchita bwino mpake akumavutika.
"Ndinkaganiza kuti pofika Pano tili ndi osewera akuluakulu nde tikaphatikiza ndi osewera akutimu yathu yaing'ono akhala atagwirana koma palibe chomwe chikuchitika nde tiziluza chonchi nkumaloza zala mphunzitsi." Anatero Mpulula.
Timuyi ikadali pa nambala yachikhumi ndi chiwiri (12) pomwe ili ndi mapointsi okwana 28 pa masewero 27 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores