"TIKAGONJA TIMAVOMEREZA" - MPULULA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Waka Waka Tigers, Leo Mpulula, wati timu yake inachita chibwana mu chigawo chachiwiri zomwe zinachititsa kuti apereke zigoli zophweka ku Silver Strikers.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Silver loweruka masana ndipo wati akagonja amangoyenera kuvomereza kuti zawavuta basi.
"Anali masewero ovuta sitinasewere bwino mchigawo chachiwiri tinagona nde tawapatsa zigoli anzathuwa tikagonja timavomereza zativuta." Anatero Mpulula.
Iye watinso anatulutsa Precious Chipungu mchigawo chachiwiri kamba koti anapempha chifukwa chovulala koma avomera kuti agonja basi.
Tigers ili pa nambala yachikhumi ndi chiwiri (12) pomwe yatolera mapointsi 19 pa masewero 18 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores