"TIKUYANG'ANA KUTSOGOLO KWATHU" - IKWANGA.
Mphunzitsi watimu ya Mzuzu City Hammers, Kondwa Ikwanga wati timu yake ikuyang'ana kutsogolo kwawo kuti awayandikire matimu omwe akutsogola ndipo akufunitsitsa chipambano mtsiku la lero.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Bangwe All Stars pa bwalo la Mzuzu mu ligi ya TNM ndipo wati chipambano ndi chofunikira kwambiri ku mbali yawo.
"Tikuyang'ana kwambiri kutsogolo kwathu chifukwa matimu omwe ali kutsogolo sitikuthawana nawo kwambiri nde tikufunitsitsa kuti tipeze chipambano chifukwa mapointsi atatu amenewa ndi ofunikira kwambiri, tikudziwa Bangwe ibwera mwa mphamvu poti inagonja koma ifeyo tikufunanso mapointsi omwewo." Anatero Ikwanga.
Timuyi ili pa nambala yachinayi mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 28 pa masewero 17 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores