"GOLOBOYI WATITHANDIZA KWAMBIRI" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Premier Bet Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wayamikira kwambiri wotchinga pagolo wawo, Donnex Mwakasinga, kuti wawathandiza kwambiri pa masewero omwe amasewera ndi Mighty Mukuru Wanderers.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 pa bwalo la Dedza ndipo wati anali masewero ovuta kwambiri omwe anayesetsa kuti apeze chigoli komabe anakanika.
"Anali masewero ovuta kwambiri, matimu onse anakonzeka kwambiri kuti mwina achite bwino mutha kuona kuti kupeza mipata kumavutanso mmasewero amenewa koma tithokozenso goloboyi wathu watipulumutsa, timayenera kupeza chipambano kutengera ndi pomwe tili koma zativuta." Anatero Bunya.
Iye wati anthu asadere nkhawa kamba koti posachedwa aywmbe kubweretsa zotsatira zabwino pomwe atha masewero anayi osapambanako.
Timuyi ikadali pa nambala yachikhumi ndi mapointsi okwana 20 pa masewero 17 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores