"CHIGAWO CHOYAMBA CHA LIGI CHAPWETEKA" - MPULULA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Tigers, Leo Mpulula, wati chigawo choyamba cha ligi yomwe ndi nthawi yomwe wakhala kutimuyi wamva kuwawa poti zinthu zambiri anazipeza zosokonekera kwambiri.
Iye amayankhula pomwe amaunikira mmene timuyi yayendera ndipo wati anayipeza timuyi yoti imachita kuvutika kuti itsale mu ligi kwa zaka zingapo ndipo kusintha zina ndi zina kumaoneka kovuta.
"Nthawi yomwe ndakhalayi ndamva kuwawa chifukwa ndinayipeza timu yoti imachita kupulumuka mu ligi mu zaka zitatuzi nde kuti usinthe zinthu komanso kaseweredwe zimavuta. Sife okhutira ndi pomwe tili, Tigers ndi timu yaikulu ikuyenera kumapezeka pabwino nde sitikugona kuti mwina zinthu zisinthe." Anatero Mpulula.
Iye wati ndi FOMO akhala masewero ovuta poti ibwera kudzapita kutsogolo kwambiri koma alimbikira kuti amalize bwino mchigawochi.
Timuyi ili pa nambala 12 mu ligi pomwe ili ndi ma pointsi 14 pa masewero 14 omwe yasewera pomwe yapambana katatu, kufanana mpha
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores