"CHIPAMBANO CHOYAMBA CHITHA KUCHIPEZA" - MWALWENI
Mphunzitsi watimu ya Baka City, Kondwani Mwalweni, wati anyamata ake akangokwanitsa kupeza chipambano chawo choyamba kukhale kuyamba kwa kuchita bwino pomwe tsopano zinthu zikuoneka zasintha kutimuyi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Bangwe All Stars ndipo wati timu yake yakonzeka bwino kuti achite bwino mmasewerowa ndipo ngati nkotheka apeze chipambano chawo choyamba.
"Masewero ndi KB anapita awa ndi masewero ena nde takonza mavuto omwe tinawaona moti apa tikayambira pompo nde tikungowalimbikitsa anyamata athu, tikangopeza chipambano choyamba kukhala kukhazikika ndithu tsogolo likuoneka lowala." Anatero Mwalweni.
Timu ya Baka City ndi yokha imene sinapezeke chipambano mu ligi ya TNM ndipo ili pansi penipeni ndi mapointsi anayi (4) pa masewero khumi omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores