"TIYESETSA KUTI TICHITE BWINO BASI" - MPULULA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Waka Waka Tigers, Leo Mpulula, wati ayiwale kaye zoti timuyi imayivutitsa timu ya Silver Strikers poti akufunika kuti alimbikire kuti apambane mmasewero awo lolemba.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe pa bwalo la Kamuzu ndipo wati akuyenera kuchilimika kuti achite bwino ndi cholinga choti asunthe pa ndandanda wa matimu amu ligi.
"Ndi masewero abwino kwambiri omwe tifunika kuti tiyesetse tichite bwino poti sili pabwino mu ligiyi nde tikufunika kuti tisinthe tikwere kumtunda. Mwina zomati Silver imavutika tikakumana tiyiwale kale, ifeyo tingopita ndi mtima woti tikawine ndipo tiyesetsa ndithu mpaka tipeze chipambano ndithu." Anatero Mpulula.
Mphunzitsiyu wati kusasewera kwa masabata awiriwa kwawapindulira poti akonza mwina ndi mwina ndipo singakhale ponamira kuti zawasokoneza.
Timu ya Tigers ili pa nambala yachikhumi ndi chiwiri (12) mu ligi ndi mapointsi Khumi ndi imodzi (11) pa masewero
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores