"TINACHINYITSA MOFULUMIRA" - MPULULA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Waka Waka Tigers, Leo Mpulula, wati timu yake siyinasewere bwino mpake yagonja kamba koti inapezetsa zigoli mofulumira kwambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-2 ndi Kamuzu Barracks pa bwalo la Kamuzu ndipo wati zinali zovuta kuti anyamata ake abwerere mu masewerowa komanso amachita chibwana.
"Sitinasewere bwino ndipo tachinyitsa zigoli mwachangu kwambiri zomwe zapangitsa kuti tisabwerere mwachangu mmasewerowa komanso taphonya mipata yochuluka nde ukamaphonya sumapambana. Si masewero oti tikanaluza koma ngati mukupanga zibwana ndi zimatere." Mpulula.
Timuyi yafika tsopano pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe ili ndi mapointsi Khumi ndi imodzi (11) pa masewero asanu ndi atatu (8) omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores