"TIMAKHALA KWAMBIRI KUMBUYO MCHIGAWO CHACHIWIRI" - MWALWENI
Mphunzitsi wogwirizira kutimu ya Baka City, Kondwani Mwalweni, wati timu yake inakhalitsa kwambiri mchigawo chawo mu chigawo chachiwiri zomwe zapangitsa kuti abwenzetse chigoli pa masewero awo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 1-1 ndi timu ya Creck Sporting Club pa bwalo la Karonga ndipo wati anthu adekhe chifukwa posachedwa apeza chipambano chawo choyamba.
"Anali masewero abwino ndipo tinayamba bwino mpaka tinapeza chigoli koma mchigawo chachiwiri anyamata anakhazikika mchigawo mwathu zomwe zinathandiza kuti tingopereka chigoli mwina tikanakhala kuti timapita kutsogolo tikanapambana." Anatero Mwalweni.
Iye wati timu yake ikadali ndi mwayi wotsala mu ligi pomwe wati tsopano anyamata ayamba kuchita bwino ndipo ayamba kupambana.
Timuyi ili pansi penipeni pa ligi pomwe yagonja kasanu ndi kufanana mphamvu katatu ndipo ali ndi mapointsi atatu pa masewero asanu ndi atatu (8).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores