"SITIKUTULUKA MU LIGI IFE" - MUYOMBE
Mphunzitsi watimu ya Baka City, Davie Muyombe, watsutsa zoti palibe chiopsezo kuti timu yake ituluka mu ligi poti wati agwiritsa ntchito mwayi pa masewero awo apakhomo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-1 ndi timu ya Mighty Waka Waka Tigers lachinayi ndipo wati timu yawo singatuluke mu ligi.
"Kutuluka ayi aah sitingatuluke, lero zinangotivuta poti osewera ena kunalibe koma tikadzakhala pakwathu sitingamachite chonchi ndipo tidzawina pakhomo." Anatero Muyombe.
Timu ya Baka City sinapambaneko masewero aliwonse mu ligiyi chilowereni pomwe yagonja kasanu ndi kufanana mphamvu kawiri ndipo ili ndi mapointsi awiri pa masewero asanu ndi awiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores