"TIKADALI NDI NTCHITO YOTI TIKONZE TIMUYI" - MPULULA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Waka Waka Tigers, Leo Mpulula, wati ali ndi ntchito yaikulu yoti agwire kutimuyi kuti ikhale bwino pomwe akufunitsitsa kuti achite bwino mu ligi ya 2024.
Mpulula amayankhula atatha masewero omwe apambana 4-1 ndi timu ya Baka City lachinayi ndipo wati ngakhale apambana, zambiri zikuyenera kukonzedwa.
"Anali masewero abwino poti tapambana masewerowa komabe ntchito ilipo yoti tikonze kuti timuyi izisewera bwino komanso mipata yochuluka nde tayiphonya nde komabe tikonza." Anatero Mpulula.
Iye wati kugoletsa zigoli zinayi zikuonetsa kuti zomwe akuwaphunzitsa osewera ake zikugwira ntchito komabe zina azizidziwa mochedwerapo.
Timuyi yafika pa nambala yachisanu pomwe ali ndi mapointsi khumi ndi imodzi (11) pa masewero asanu ndi awiri (7).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores