"TIKUPHONYA MIPATA YOCHULUKA" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Abbas Makawa, wati timu yake inaphonya mipata yochuluka yomwe yachititsa kuti agonje pomwe amakumana ndi Kamuzu Barracks.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-1 ndi timu ya KB ndipo wati timu yake inayesetsa kuti achite bwino koma wawamvetsetsa anyamata ake ndipo akonza.
"Anali masewero abwino kwambiri, tasewera bwino ndipo mipata tinayipeza koma chikusowa ndi kungogwetseramo mu golomo koma awanso ndi anthu, amakhala ndi zofooka ndipo tawamvetsetsa tikonza kuti tichite bwino mmasewero akudza." Anatero Makawa.
Iye anadandaulanso ndi kayimbilidwe ponena kuti oyimbira amapanga ziganizo zokomera KB ndipo iye sanakhutitsidwe nazo.
Timu ya Civo ili pa nambala 11 pomwe yatolera mapointsi atatu okha pa masewero anayi omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores