"TIMAFUNIKA KUPAMBANA TIKAKHALA PAKHOMO" - CHIMKWITA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Karonga United, Chris Chimkwita, wati kupeza chipambano pa masewero awo a lamulungu ndi chabwino kamba koti asunthapo pa ndandanda wa matimu mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Mighty Waka Waka Tigers 3-1 ndipo wati zimakhala bwino kumapeza chipambano pa khomo pamaso pa abale.
"Anali masewero abwino ndipo anyamata anayesetsa kuti tichite bwino zathekadi Pano panali makolo athu, abale athu, akazi athu, zibwezi za osewerawa nde pamafunika kuti tipeze chipambano." Anatero Chimkwita.
Iye wati penate yomwe anapatsidwa a timu ya Tigers inali yongowapatsa kamba zoti sinali yeniyeni komabe anakondwera ndi chipambano chimenechi.
Timu ya Karonga ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe ili ndi mapointsi 7 pa masewero anayi omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores