"ANYAMATA ENA AKUNGOWONJEZERA NAMBALA" - KAFOTEKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Elvis Kafoteka, wadandaula kuti osewera ena mutimuyi sakulimbikira ndi chifukwa chake akulephera kupeza zotsatira zabwino.
Iye amayankhula atagonja 1-0 ndi timu ya FOMO ku Mulanje ndipo wati anyamata ena sakumachita zimene awuzidwa zomwe zamudandaulitsa kwambiri.
"Penanso ndikumadabwa kuti kodi akufuna kuti Kochi alowe yekha chifukwa anyamata ena mtima alibe nde Izizi sizilibwino, ena akungochulukitsamo nambala nde sitingamachite bwino tikuyenera kukonza zimenezi." Anatero Kafoteka.
Timuyi ili pa nambala 12 mu ligi pomwe yapambana masewero amodzi okha ndi kugonja atatu kuti akhale ndi mapointsi atatunso pa masewero anayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores