"TIKHALA NDI TIMU YABWINO" - KAFOTEKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Elvis Kafoteka, wati timu yake ikhale imodzi mwa matimu oopsa kwambiri pomwe izisewera mpira wapamwamba kwambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 0-3 pa bwalo la Karonga lamulungu ndipo wati timu yake inasokonekera mchigawo chachiwiri mpake inapezetsa zigoli zambiri.
"Anali masewero abwino kwambiri pomwe tinasewera bwino mchigawo choyamba koma mchigawo chachiwiri tinafooka kwambiri mpake tinapezetsa zigolizo koma ndi mmene tasewerera mchigawo choyamba ndikulimba mtima kuti timuyi ikhala bwino." Anatero Kafoteka.
Timu ya Chitipa ili pa nambala 11 mu ligi ya TNM pomwe yatolera mapointsi atatu pa masewero atatu omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores