"TINALI NDI PHUMA POTI TALUZA KWAMBIRI" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Christopher Nyambose, wati kufanana mphamvu ndi Karonga United ndi chimodzimodzi kugonja kumene pomwe amayenera kupambana chifukwa anali pakhomo.
Nyambose amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 1-1 ndi Karonga United pa bwalo la Mpira ndipo wati anyamata ake amachita phuma loti achite bwino poti anagonja mmasewero awiri awo oyamba.
"Anali masewero ovuta kwambiri kutengera kuti tonse tinali ovutika okhaokha koma timayenera kupambana komabe takanika kuteteza chigoli chathu. Ndikuona kuti kugonja mmasewero awiri aja kwawapatsa anyamata phuma kuti azisewera mofuna kupambana nanga si masapota akumayankhula nde mwina zikumawapangitsa kuphonya kwambiri." Anatero Nyambose.
Timuyi tsopano ili pansi pa ligiyi ndi point imodzi pa masewero atatu omwe yasewera ndipo ikumana ndi Mighty Mukuru Wanderers mmasewero awo otsatira.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores