"TIKUYENERA KUKONZA ZAMBIRI" - MPULULA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Waka Waka Tigers, Leo Mpulula, wati timu yake ikufunika kukonzedwa mu zinthu zambiri angakhale kuti apambana pomwe wati siwokhutira ndi mmene amasewerera osewera ake.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Mzuzu City Hammers 1-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati chipambanochi chakhala bwino pokonza mmene aonekere pa ndandanda wa matimu koma ali ndi ntchito yaikulu yokonza timuyi.
"Tithokoze osewera kuti tapambana koma tataya mipata yochuluka kwambiri zomwe zikutanthauza kuti tili ndi ntchito yaikulu yoti tikonze pa osewerawa komabe timafunika kuti tipambane kuti zisaipe pa tebulo koma ntchitoyo ndi yambiri yoti tikonze." Anatero Mpulula.
Tigers tsopano ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe yatolera mapointsi anayi (4) pa masewero atatu omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores