BULLETS SIPITANSO KU MOZAMBIQUE
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalengeza kuti ulendo wawo wopita mdziko la Mozambique walephereka.
Timuyi inali pa pangano loti ikukasewera ndi timu ya UD Songo koma zakanika kamba koti osewera ena sapezeka ku timuyi.
Timuyi yatumiza osewera okwana asanu ndi anayi kutimu ya dziko lino ndipo asewera mu mpikisano wa mayiko anayi omwe uyambe pa 21 March 2024.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores