"NDANDANDA WONSE UTULUKA LACHISANU" - MABEDI
Mphunzitsi watimu ya Flames, Patrick Mabedi, wati atulutsa ndandanda wa osewera omwe agwiritse ku mpikisano wa matimu anayi omwe uchitikire ku Lilongwe kuyambira pa 21 March lachisanu likudzali.
Iye amayankhula kutsatira mayere omwe aonetsa kuti timu ya Malawi iyamba kusewera ndi dziko la Kenya mu ndime ya matimu anayi ndipo wati akumana ndi timu yabwino.
"Tatola timu yabwino yomwe itipatsenso zomwe timafuna. Ndi ya njala poti yakhala isakusewera mipikisano nde nawo adzalimbikira kuti ayese osewera awo." Anatero Mabedi.
Iye wati akukambirana ndi matimu onse omwe kumasewera osewera aku Malawi ndipo akamaliza atulutsa ndandanda wotsiriza wa timuyi. Iye wathokozanso omwe akonza mpikisanowu ponena kuti ndi wa phindu kwambiri.
"Tatengako osewera ena oti sitingawayese pa masewera a World Cup qualifiers kapena AFCON osawayesa nde mpikisanowu utipatsa mpata owaoneratu osewerawo komanso akhala ndi mpata wozikonzekeretsa pa masewero ndi matimu ak
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores