WANDERERS YACHOTSA MPINGANJIRA
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yachotsa ntchito mkulu watimuyi (CEO), a Roosevelt Mpinganjira kuyambira loweruka masana.
A Mpinganjira atsimikiza okha za kuchotsedwaku koma sanafotokoze zambiri pankhaniyi.
Ena mwa akuluakulu atimuyi sanalinso opezeka kuti ayankhulepo pa nkhaniyi.
Mpinganjira wakhala kutimuyi kwa miyezi isanu ndi itatu yokha chimulembereni ndipo anali yekha wotsalapo pomwe Manoma anathetsa komiti yawo yonse mwezi watha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores