BULLETS YAKASUMA KU SRFA
Masewero omwe amayenera kukhalako lachinayi pakati pa FOMO FC komanso Zingwangwa United ayimitsidwa kaye pomwe bungwe la Southern Region Football Association likufufuza dandaulo la FCB Nyasa Big Bullets.
Bullets yakadandaula ku bungweli ati kamba koti osewera atatu a Zingwangwa anasewera ali ndi makadi achikasu awiri zomwe ndi zosaloledwa.
Iyo yati osewerawa ndi Zewu Nyaka, Madalo Tambula komanso Vitumbiko Nyirenda ndipo samayenera kusewera mmasewero achibwerenza omwe anagonja 1-2 pa bwalo la Kamuzu.
Mwa ichi, SRFA layamba kufufuza ndipo masewero ena pakati pa Ntopwa Airbase ndi Ntopwa apitilirabe. Nako ku chigawo chapakati, masewero otsiriza anaimitsidwa kamba koganizira zachinyengo.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores