NGINDE AKHONZA KULOWERA KU MANOMA
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Macdonald Mtetemera, wakhala nawo mu gulu la aphunzitsi omwe akumveka kuti timu ya Mighty Mukuru Wanderers ikhonza kuwatenga kuti atsogolere timuyi mu 2024.
Izi zadza pomwe Manoma alibe mphunzitsi kutsatira kuchoka kwa Mark Harrison ndipo iwo alowa mu chipwilikiti chofuna mphunzitsi woti alowe mmalo kutimuyi.
Kupatula Mtetemera, Meke Mwase wakale wa Flames, Alex Ngwira komanso Eliya Kananji ndi omwe akumveka zotenga ntchito yovutitsitsa kwambiri mdziko muno ngati mmene ananenera akuluakulu atimuyi.
Mtetemera waonekera kwambiri mu chaka cha 2023 pomwe wachita bwino kwambiri ndi timu yomwe inali zoti yangolowa kumene ya Chitipa United.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores