"ZIGOLI TANGOWAPATSA MPAKE ZATIVUTA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati anyamata ake sanali bwino kwambiri pomwe amalakwitsa ndipo zigoli zonse angowapatsa a Bangwe All Stars komabe ayesetsa kuti chaka cha mawa adzafikenso ndi mphamvu.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi Bangwe All Stars pa bwalo la Mpira lamulungu ndipo wati timu yake sinasewere bwino kwambiri.
"Sitinali bwino anyamata anachotsa chidwi makamaka kumbuyo kwathu mutha kuona kuti tangowapatsa zigoli zija, china tazichinya china penate nde zativuta basi. Tinalibe timu yolimba kwambiri mwina ndi zomwe zimativuta koma chaka cha mawa titolerabe kuti mwina tikhale ndi osewera oti titha kumaliza nawo ligi yonse." Anatero Kajawa.
Kugonjaku kwapangitsa timuyi kuti ituluke mu ndandanda wa matimu asanu ndi atatu (8) pomwe yathera pa nambala 9 ndi mapointsi 38 pa masewero 30 mu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores