BULLETS RESERVE YAKANIKA KUBWERA PAMWAMBA
Akatswiri omwe akuteteza ligi yakummwera kwa dziko lino ya Thumbs Up Southern Region Football league, FCB Nyasa Big Bullets Reserve, akanika kufika pa mwamba pa ligiyi pomwe yagonja 2-0 ndi timu ya Waka Waka Tigers Reserve pa bwalo la Kamuzu lolemba masana
Timuyi inali ndi mwayi ofika pamwamba kutsatira kugonja kwa timu ya FOMO FC 1-0 ndi timu ya The Boys lamulungu ndipo inaona ngati kutulo pomwe Tigers yomwe ikuvutika mu ligi yawamenya pakhomo pawo pomwepo.
Timuyi yataya mapointsi asanu mmasewero awiri omwe yasewera mmasabata awiri apitawa pomwe anafanananso mphamvu ndi timu ya The Boys 1-1 sabata yatha.
FOMO ilamulirabe mu gulu B la ligiyi ndi mapointsi 29 pa masewero 13 pomwe Bullets Reserve ili pachiwiri ndi mapointsi 26 pa maseweronso 14, Ntopwa ili ndi 23 pomwe Zomba Airbase ili ndi 21 mu gulu lomweli.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores