KHUDA WAYAMBA ZOKONZEKERA KU SYRIA
Katswiri wa timu ya Flames komanso wakale wa Polokwane City, Khuda Myaba wayambapo kuchita zokozekera ndi timu yake yatsopano ya Tishreen SC yaku Syria.
Izi zili chomwechi pomwe timuyi yalengeza loweruka kuti yatenga ntchito za katswiriyu ndipo inamuonetsa kwa anthu.
Muyaba yemwe ali ndi dzaka 29, mu mchaka cha 2019 anakhalapo katakwe omwetsa zigoli mu ligi ya TNM pomwe anachinya zigoli 21 ali ku timu ya Silver Strikers.
Tishreen SC inayambitsidwa mu mchaka cha 1947 ndipo imasewera mumpikisano wa Syria Premier League komanso mu Arab Club Champions Cup. Iyo yatenga ukatswiri wadzikolo kokwana kasanu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores