"TAKHUTIRA NDI KUFANANA MPHAMVU" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati ndi wokhutira ndi kufanana mphamvu ndi timu ya Bangwe All Stars pomwe wati kubwerera ndi point imodzi ku Blantyre ndi chamuna chomwe.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anafanana mphamvu 1-1 pa bwalo la Mpira ndipo wati wakondwa ndi anyamata ake poti anakwanitsa kubwenza chigoli chomwe Bangwe inapeza.
"Ndife okhutira kwambiri ndi mmene masewerowa athera. Tinayamba bwino pomwe tinamenya pagolo kwambiri kuposa Bangwe koma anawapatsa penate komabe tinawalimbikitsa osewera mpaka akwanitsa kupeza chigoli nde kufanana mphamvu ndi zotsatira zabwino koyenda." Anatero Kaunda.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe ili ndi mapointsi anayi pa masewero atatu omwe yasewera.
MUTUMIZILE KU 0981511741
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores