Timu ya Blue Eagles ikupitilira kudandaula ndi momwe bungwe la Super League of Malawi (Sulom) ikuyendesera ligiyi maka poika masewero.
Malingana ndi Blue Eagles, Sulom inasintha masewero a Bullets a Loweluka kuwaika Lachisanu ndi cholinga choti osewera onse a timuyi kuphatikiza omwe ali ndi Flames asewere nawo masewero-wa.
Malingana ndi timu ya apolisi-yi, ngakhale kuti osewera awo atatu (Schumacher Kuwali, Micium Mhone komanso Sankhani Mkandawire) ali ndi timu ya Malawi, akuwapasa masewero sabata ya mawa.
Iwo ati ndi zodandaulitsa kaamba koti osewera awo ena kukhala kulibe pa masewero awo ndi TN Stars.
Aka ndi kachiwiri timu ya Blue Eagles kudandaula ndi momwe Sulom ikuikira masewero ake amu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores